Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu, ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu.
Masalimo 108:4 - Buku Lopatulika Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pakuti chikondi chanu chosasinthika nchachikulu, chofika mpaka pamwamba pa mlengalenga, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kutalika kwake kuposa kumwamba; kukhulupirika kwanu kumafika mlengalenga. |
Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu, ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu.
Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye.
Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka; mudzakhazika chikhulupiriko chanu mu Mwamba mwenimweni.
Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.
Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.