Masalimo 108:3 - Buku Lopatulika Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova: ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova: ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a m'maiko onse, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzakutamandani Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba za Inu pakati pa anthu a mitundu ina. |
Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.
Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
Imba, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu.
Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.