Masalimo 108:12 - Buku Lopatulika Tithandizeni mumsauko; pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tithandizeni mumsauko; pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo, pakuti chithandizo cha munthu nchopandapake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tithandizeni ife kulimbana ndi mdani, pakuti thandizo la munthu ndi lopanda pake. |
Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?
Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.
Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo chabe; kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.