Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.
Masalimo 108:1 - Buku Lopatulika Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu, mtima wanga wakonzekadi! Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda. Lumpha, iwe mtima wanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu; ndidzayimba nyimbo, inde ndidzayimba nyimbo zotamanda ndi moyo wanga wonse. |
Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera kunthawi za nthawi.
Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.
Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.
Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.