Masalimo 104:9 - Buku Lopatulika Munaika malire kuti asapitirireko; kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munaika malire kuti asapitirireko; kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Madziwo Inu mudaŵaikira malire oti asabzole, kuti asaphimbenso dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa, iwo sadzamizanso dziko lapansi. |
Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso padziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.
Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.