Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 104:4 - Buku Lopatulika

Amene ayesa mphepo amithenga ake; lawi la moto atumiki ake;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Amene ayesa mphepo amithenga ake; lawi la moto atumiki ake;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mphepo mumazisandutsa amithenga anu, malaŵi amoto mumaŵasandutsa atumiki anu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Amapanga mphepo kukhala amithenga ake, malawi amoto kukhala atumiki ake.

Onani mutuwo



Masalimo 104:4
8 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu.


Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.


moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu; mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake;


Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makala amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unachita cheza, ndi m'motomo mudatuluka mphezi.


Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakutuluka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.


Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri.


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


Ndipo za angelo anenadi, Amene ayesa angelo ake mizimu, ndi omtumikira Iye akhale malawi amoto.