Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 104:2 - Buku Lopatulika

muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mumadzifunditsa ndi kuŵala ngati chovala, mwatambasula mlengalenga ngati hema.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala; watambasula miyamba ngati tenti

Onani mutuwo



Masalimo 104:2
11 Mawu Ofanana  

Taonani, Iye ayala kuunika kwake pamenepo. Navundikira kunsi kwake kwa nyanja.


Woyala thambo yekha, naponda pa mafunde a panyanja.


Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;


Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.


Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka.


Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika; anali nayo mitsitsi ya dzuwa yotuluka m'dzanja lake, ndi komweko kunabisika mphamvu yake.


Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake;


ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.


amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.


Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.