Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza; inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni.
Masalimo 104:16 - Buku Lopatulika Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mitengo ya Chauta amaithirira ndi madzi ambiri, mikungudza ya ku Lebanoni imene adaibzala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino, mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala. |
Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza; inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni.
paphiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko aliwonse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.
Ziyalika monga zigwa, monga minda m'mphepete mwa nyanja, monga khonje wooka Yehova, monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.