Masalimo 104:10 - Buku Lopatulika Atumiza akasupe alowe m'makwawa; ayenda pakati pa mapiri: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Atumiza akasupe alowe m'makwawa; ayenda pakati pa mapiri: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mumatumphutsa akasupe m'zigwa, mitsinje imayenda pakati pa mapiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa; madziwo amayenda pakati pa mapiri. |
Ndipo mchenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.
Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti see, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa chipululu, chikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi.
Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe ndi la maiwe akutuluka m'zigwa, ndi m'mapiri;