Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Masalimo 104:1 - Buku Lopatulika Lemekeza Yehova, moyo wanga; Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lemekeza Yehova, moyo wanga; Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri. Mumavala ulemu ndi ufumu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri; mwavala ulemerero ndi ufumu. |
Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Ochimwa athedwe kudziko lapansi, ndi oipa asakhalenso. Yamika Yehova, moyo wanga. Aleluya.
Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu; mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse;
Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.
Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.
Ndipo anavala chilungamo monga chida chapachifuwa, ndi chisoti cha chipulumutso pamutu pake; navala zovala zakubwezera chilango, navekedwa ndi changu monga chofunda.
Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.
Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka.
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu,
Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.