woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
amene muchitira chifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'chifukwa cha ana ao a pambuyo pao, dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu;
ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.
Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.
Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.
Yehova ndiye wolekereza, ndi wa chifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula wopalamula; wakuwalanga ana chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.