ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
Masalimo 103:7 - Buku Lopatulika Analangiza Mose njira zake, ndi ana a Israele machitidwe ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Analangiza Mose njira zake, ndi ana a Israele machitidwe ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adadziŵitsa Mose njira zake, adaonetsa Aisraele ntchito zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anadziwitsa Mose njira zake, ntchito zake kwa Aisraeli. |
ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao;
Iye analankhula nao mu mtambo woti njo: Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa.
Ndipo Yehova anatsikira paphiri la Sinai, pamutu pake paphiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu paphiri; ndi Mose anakwerapo.
Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.
Ndipo sanaukenso mneneri mu Israele ngati Mose, amene Yehova anadziwana naye popenyana maso;