Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Masalimo 103:6 - Buku Lopatulika Yehova achitira onse osautsidwa chilungamo ndi chiweruzo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova achitira onse osautsidwa chilungamo ndi chiweruzo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta amaweruza mwachilungamo onse opsinjidwa amaŵachitira zolungama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova amachita chilungamo ndipo amaweruza molungama onse opsinjika. |
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwowa kumabwalo a milandu?