Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso.
Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake.
koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso ndipo malo ake sakumbukirikanso.
ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga.
Koma munthu akufa atachita liondeonde inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti?
Diso lidamuonalo silidzamuonanso; ndi malo ake sadzampenyanso.
Mau a wina ati, Fuula. Ndipo ndinati, Kodi ndifuule chiyani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo;
udzu unyala, duwa lifota; chifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu.