Kodi Mulungu sakhala m'mwamba m'tali? Ndipo penyani kutalika kwake kwa nyenyezi, zili m'talitali.
Masalimo 103:11 - Buku Lopatulika Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa; |
Kodi Mulungu sakhala m'mwamba m'tali? Ndipo penyani kutalika kwake kwa nyenyezi, zili m'talitali.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
Pakuti chifundo chake cha pa ife ndi chachikulu; ndi choonadi cha Yehova nchosatha. Aleluya.
Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.
Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.
Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka; mudzakhazika chikhulupiriko chanu mu Mwamba mwenimweni.
Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.