Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere;
Masalimo 103:10 - Buku Lopatulika Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero satichitira molingana ndi machimo athu, kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu. |
Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere;
Ndipo mwa nsoni zanu zochuluka simunawathe, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa chisomo ndi chifundo.
nakufotokozere zinsinsi za nzeru, popeza zipindikapindika machitidwe ao! Chifukwa chake dziwa kuti Mulungu akuiwalira mphulupulu zina.
Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindule nako.
Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.