Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Masalimo 103:1 - Buku Lopatulika Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamanda Yehova, iwe moyo wanga; ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera. |
Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.
Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.
Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.
Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.
Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m'chidziwitso, ndi kuzindikira konse;
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.