Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
Masalimo 102:27 - Buku Lopatulika Koma Inu ndinu yemweyo, ndi zaka zanu sizifikira kutha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Inu ndinu yemweyo, ndi zaka zanu sizifikira kutha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Inu simusintha, zaka zanu sizitha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Inu simusintha, ndipo zaka zanu sizidzatha. |
Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
Pakuti pamaso panu zaka zikwi zikhala ngati dzulo, litapita, ndi monga ulonda wa usiku.
Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.