Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
Masalimo 102:24 - Buku Lopatulika Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga: Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga: Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikuti, “Mulungu wanga, musandichotse tsopano ndisanakalambe, Inu amene zaka zanu sizitha mpaka muyaya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Ine ndinati: “Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga; zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse. |
Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.
Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?
Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.
Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri mu Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake;
Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.