Pakuti chomsamalitsa nyumba yake nchiyani, atapita iye, chiwerengo cha miyezi yake chitadulidwa pakati?
Masalimo 102:23 - Buku Lopatulika Iye analanda mphamvu yanga panjira; anachepsa masiku anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye analanda mphamvu yanga panjira; anachepsa masiku anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta wathyola mphamvu zanga ndisanakule, wafupikitsa masiku anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anathyola mphamvu zanga pa nthawi ya moyo wanga; Iyeyo anafupikitsa masiku anga. |
Pakuti chomsamalitsa nyumba yake nchiyani, atapita iye, chiwerengo cha miyezi yake chitadulidwa pakati?
Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.
Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa mu Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera mu Yerusalemu.
Pa nthawi yomweyo adzatcha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.