Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.
Masalimo 102:20 - Buku Lopatulika kuti amve kubuula kwa wandende; namasule ana a imfa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti amve kubuula kwa wandende; namasule ana a imfa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa kuti amve kubuula kwa anthu am'ndende, kuti aŵapulumutse amene adaayenera kuphedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti amve kubuwula kwa anthu a mʼndende, kuti apulumutse amene anayenera kuphedwa.” |
Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.
M'mzinda waukulu anthu abuula alinkufa; ndi moyo wa iwo olasidwa ufuula; koma Mulungu sasamalira choipacho.
ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.
Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu; monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale.
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
amene anapululutsa dziko, napasula mizinda yake, amene sanamasule ndende zake, zinke kwao?
Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitsani anthu anu Israele, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.