Penyetsetsani malinga ake, yesetsani zinyumba zake; kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.
Masalimo 102:18 - Buku Lopatulika Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mbadwo wakutsogolo, kuti anthu amene mpaka tsopano lino sanabadwebe, nawonso adzatamande Chauta, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo, kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova: |
Penyetsetsani malinga ake, yesetsani zinyumba zake; kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.
Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.
yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.
chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri.
koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake.
Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.
Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.