Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
Masalimo 102:17 - Buku Lopatulika anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzayankha pemphero la anthu ake otayika, sadzanyoza kupemba kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo. |
Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.
mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.
Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeretsa; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, mu Yerusalemu.
Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.
Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha.
ndipo ulemerero wa Yehova udzavumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena chomwecho.
Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.
Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mzindawu udzamangidwira Yehova kuyambira pa Nsanja ya Hananele kufikira ku Chipata cha Kungodya.
Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.
Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.