Masalimo 102:11 - Buku Lopatulika Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Masiku anga ali pafupi kutha ngati mthunzi wamadzulo. Ndikufota ngati udzu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo; Ine ndikufota ngati udzu. |
Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?
inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.
Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;