Koma ngati mumuka, chitani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.
Masalimo 102:10 - Buku Lopatulika chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu; popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu; popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa chifukwa cha ukali wanu ndi mkwiyo wanu, popeza kuti Inu mwandinyamula ndi kunditaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero chifukwa cha ukali wanu waukulu, popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali. |
Koma ngati mumuka, chitani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.
Mumnofu mwanga mulibe chamoyo chifukwa cha ukali wanu; ndipo m'mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa.
Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.
Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndinkapita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.
Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.
Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;