Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
Masalimo 10:18 - Buku Lopatulika kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa, ndi cholinga chakuti munthu amene ali wa dziko lapansi asaopsenso. |
Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.
Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.
Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.