Masalimo 10:15 - Buku Lopatulika Thyolani mkono wa woipa; ndipo wochimwa, mutsate choipa chake kufikira simuchipezanso china. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Thyolani mkono wa woipa; ndipo wochimwa, mutsate choipa chake kufikira simuchipezanso china. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Thetsani mphamvu za munthu woipa ndi wochimwa. Fufuzani kuipa kwake, ndipo mumlange kuti asadzabwerezenso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Thyolani dzanja la woyipitsitsa ndi la munthu woyipa; muzengeni mlandu chifukwa cha zoyipa zake zimene sizikanadziwika. |
Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.
Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.
Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeze pakuboola, koma ponsepo.
Momwemo ndidzaleketsa dama m'dzikomo, kuti alangizidwe akazi onse kusachita monga mwa dama lanu.
Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.
Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.