Masalimo 10:11 - Buku Lopatulika Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumtima mwake amaganiza kuti, “Mulungu sasamalako, waphimba maso ake, sadzaziwona zimenezi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amati mu mtima mwake, “Mulungu wayiwala, wabisa nkhope yake ndipo sakuonanso.” |
Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani?
Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha; chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.
Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.
Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.
Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mzindawo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.
Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.
Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.