Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.
Marko 9:6 - Buku Lopatulika Pakuti sanadziwe chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti sanadziwe chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ankatero chifukwa chosoŵa chonena, pakuti iye ndi anzake aja anali atagwidwa ndi mantha aakulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Iye sanadziwe choti anene, anali ndi mantha akulu). |
Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.
Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munatuluka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.
Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.
Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,