Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.
Marko 9:5 - Buku Lopatulika Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Petro anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, ndi kwabwino kuti ife tili pano. Tiyeni timange misasa itatu; umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.” |
Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.
Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pano misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.
Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;
Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.