Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Marko 9:11 - Buku Lopatulika Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adamufunsa kuti, “Nanga bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Eliya adzayenera kuyamba wabwera?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anamufunsa Iye kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kuyamba wabwera?” |
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.