Marko 8:8 - Buku Lopatulika Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo madengu asanu ndi awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo madengu asanu ndi awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nadzaza madengu asanu ndi aŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. |
Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.
Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzala.
Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya anthu zikwi zinai, ndi madengu angati munawatola?
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.