Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.
Marko 8:7 - Buku Lopatulika Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaalinso ndi tinsomba toŵerengeka. Yesu adathokoza Mulungu chifukwa cha tinsombato, nalamula ophunzira ake kuti atiperekenso kwa anthu aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. |
Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.
Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.
Ndipo uyang'aniranji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira?