Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.
Marko 8:22 - Buku Lopatulika Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Betsaida. Kumeneko anthu adabwera ndi munthu wakhungu, napempha Yesu kuti amchiritse pomkhudza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. |
Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.
ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.
Ndipo anamkhudza dzanja lake, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.
Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka.
pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze.
Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.
Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika mu Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa.
Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumzinda dzina lake Betsaida.
Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa mu Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.