Marko 8:18 - Buku Lopatulika Pokhala nao maso simupenya kodi? Ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pokhala nao maso simupenya kodi? Ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maso muli nawo, kodi simuwona? Ndipo makutu muli nawo, kodi simumva? Kodi inu simukukumbukira zijazi? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira? |
Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse.
Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;
Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.
kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.
Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse.
monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.
koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.
Mwa ichi sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m'choonadi chili ndi inu.