Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.
Marko 8:16 - Buku Lopatulika Ndipo anatsutsana wina ndi mnzake, nanena kuti, Tilibe mikate. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatsutsana wina ndi mnzake, nanena kuti, Tilibe mikate. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo ophunzirawo adayamba kukambirana nkumati, “Akuterotu chifukwa tilibe buledi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.” |
Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.
Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? Kodi muli nayo mitima yanu youma?
Ndipo anatsutsana mwa okha, nanena, Ngati tinena uchokera Kumwamba; adzati, Simunamkhulupirire chifukwa ninji?