Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.
Marko 8:12 - Buku Lopatulika Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adadzumira mu mtima nati, “Kodi bwanji anthu a mbadwo uno amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa? Ndithu ndikunenetsa kuti anthu a mbadwo unowu sadzachiwona chizindikiro akufunacho.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.” |
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.
Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona chizindikiro cha Inu.
Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo.
Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.
Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.
Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.