Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;
Marko 7:6 - Buku Lopatulika Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵayankha kuti, “Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaalemba kuti, “ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutalitali ndi Ine. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayankha kuti, “Yesaya ananena zoona pamene ananenera za inu achiphamaso; monga kunalembedwa kuti: “Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. |
Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;
Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.
Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso.
Koma popeza sanavomerezane, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu,
akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.
Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.