Marko 7:24 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adanyamuka kupita ku dera la ku Tiro. Adakakhala kunyumba kwina, ndipo sadafune kuti anthu adziŵe kuti ali kumeneko. Komabe sadathe kubisika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anachoka kumalo amenewo napita ku madera a Turo. Iye analowa mʼnyumba ndipo sanafune wina kuti adziwe zimenezi; komabe sanathe kudzibisa. |
Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa.
Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
Ndipo Iye anati, Iwe sudzakondwanso konse, iwe namwali wovutidwa, mwanawamkazi wa Sidoni; uka, oloka kunka ku Kitimu; ngakhale kumeneko iwe sudzapumai.
Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,
Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.
Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.
Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake.
Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli.
Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizingathe kubisika.