kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.
Marko 7:23 - Buku Lopatulika zoipa izi zonse zituluka m'kati, nkudetsa munthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 zoipa izi zonse zituluka m'kati, nizidetsa munthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu.” |
kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.
Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;
zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:
Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika.
Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.
Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao.
Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero.