Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake.
Marko 7:22 - Buku Lopatulika zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. |
Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake.
Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.
Ungakhale ukonola chitsiru m'mtondo ndi munsi, pamodzi ndi mphale, koma utsiru wake sudzamchoka.
Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;
ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.
Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosachimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi chipasuko zili m'njira mwao.
Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?
Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Chifukwa chake ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukulu ndithu!
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
Dzichenjerani, mungakhale mau opanda pake mumtima mwanu, ndi kuti, Chayandika chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka cha chilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale tchimo.
Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, diso lake lidzaipira mbale wake, ndi mkazi wa pa mtima wake, ndi ana ake otsalira;
Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi;
Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa;
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.