Marko 7:19 - Buku Lopatulika chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu sichiloŵa mumtima mwake, koma m'mimba, pambuyo pake nkumakatayidwa ku thengo.” (Pakunena zimenezi, Yesu adagamula kuti zakudya zonse anthu angathe kuzidya.) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti sikalowa mu mtima wake koma mʼmimba mwake, ndipo kenaka kamatuluka kunja.” (Ndi mawu amenewa, Yesu anayeretsa zakudya zonse). |
Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;
Ndipo mau anamdzeranso nthawi yachiwiri, Chimene Mulungu anayeretsa, usachiyesa chinthu wamba.
Koma mau anayankha nthawi yachiwiri otuluka m'mwamba, Chimene Mulungu anachiyeretsa, usachiyesera chinthu wamba.
Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;
Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m'chakudya, kapena chakumwa, kapena m'kunena tsiku la chikondwerero, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;