Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Marko 7:14 - Buku Lopatulika Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Yesu adaitananso anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani nonsenu, ndipo mumvetse bwino. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, “Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi. |
Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
Ndipo Iye anati, Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang'anani inu ndithu, koma osadziwitsa.
amene mneneri Yeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, kuti,
muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita.
kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.
Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.
Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga?