Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.
Marko 7:13 - Buku Lopatulika muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakutero mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe, chifukwa cha mwambo wanu umene mumasiyirana. Ndipo mumachita zinanso zambiri zotere.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.” |
Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.
Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zochimwa zonse adazichita atate wake, naopa wosachita zoterezo,
Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo.
iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.
Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:
Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu;
Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?
ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.
njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.