Lankhula ndi ana a Israele, nunene nao, Aliyense mwa inu akabwera nacho chopereka cha kwa Yehova, muzibwera nacho chopereka chanu chikhale cha zoweta, cha ng'ombe, kapena cha nkhosa, kapena cha mbuzi.
Marko 7:11 - Buku Lopatulika koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake, Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake, Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni zasanduka Korobani,” (ndiye kuti zoperekedwa kwa Mulungu), Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), |
Lankhula ndi ana a Israele, nunene nao, Aliyense mwa inu akabwera nacho chopereka cha kwa Yehova, muzibwera nacho chopereka chanu chikhale cha zoweta, cha ng'ombe, kapena cha nkhosa, kapena cha mbuzi.
Koma inu munena, Aliyense amene anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu;
Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mtulo wa pamwamba pake wadzimangirira.
Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi.