Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Marko 7:10 - Buku Lopatulika Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja Mose adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Mose anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako,’ ndipo, ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ |
Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake.
Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.
Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako.
Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.