kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.
Marko 6:9 - Buku Lopatulika koma avale nsapato; ndipo anati, Musavale malaya awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma avale nsapato; ndipo anati, Musavale malaya awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nsapato muvale inde, koma musakhale ndi mikanjo iŵiri.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Muvale nsapato koma osatenga malaya apadera. |
kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Ndipo ananena nao, Kumene kulikonse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukachokako.
ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao;
Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'chuuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo ananena naye, Funda chovala chako, nunditsate ine.