Marko 6:8 - Buku Lopatulika ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaŵalamula kuti, “Musatenge kanthu kena kalikonse pa ulendo, koma ndodo yokha. Musatenge kamba, kapena thumba lapaulendo, kapena ndalama m'chikwama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama. |
Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira.
Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nao malaya awiri.