Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mzindawo Zowari.
Marko 6:5 - Buku Lopatulika Ndipo kumeneko sanakhoze Iye kuchita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ake pa anthu odwala owerengeka, nawachiritsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kumeneko sanakhoze Iye kuchita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ake pa anthu odwala owerengeka, nawachiritsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero sadathe kuchita zinthu zamphamvu kumeneko. Adangosanjika manja pa odwala oŵerengeka, nkuŵachiritsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sanachite zodabwitsa kumeneko, koma anangosanjika manja pa odwala ochepa ndi kuwachiritsa. |
Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mzindawo Zowari.
Ndipo pamene anaona kuti sanamgonjetse, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye.
nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo.
Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa.
Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindule nao mau omvekawo, popeza sanasakanizike ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva.