Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.
Marko 5:9 - Buku Lopatulika Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; chifukwa tili ambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; chifukwa tili ambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine ‘Chigulu,’ chifukwa tilipo ochuluka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anamufunsa iye, “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Dzina langa ndine Legiyo, pakuti tilipo ambiri.” |
Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono.
Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?
Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.
Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.